Song of Solomon 6

Abwenzi

1Iwe wokongola kuposa akazi onsewa,
kodi wokondedwa wakoyo wapita kuti?
Kodi wokondedwa wakoyo wakhotera njira iti
kuti timufunefune pamodzi ndi iwe?
Mkazi

2Wachikondi wanga watsikira ku munda kwake,
ku timinda ta zokometsera zakudya,
akukadyetsa ziweto zake ku minda,
ndiponso akuthyola maluwa okongola.
3Wokondedwa wangayo ndine wake ndipo iyeyo ndi wangawanga;
amadyetsa ziweto zake pakati pa maluwa okongola.
Mwamuna

4Ndiwe wokongola, bwenzi langa, ngati Tiriza,
wokongola kwambiri ngati Yerusalemu,
ndiwe woopsa ngati gulu lankhondo lonyamula mbendera.
5Usandipenyetsetse;
pakuti maso ako amanditenga mtima.
Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi
zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.
6Mano ako ali ngati gulu la nkhosa
zimene zikubwera kuchokera kokazisambitsa,
iliyonse ili ndi ana amapasa,
palibe imene ili yokha.
7Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba kumutu,
masaya ako ali ngati mabandu a makangadza.
8Ngakhale patakhala akazi a mfumu 60,
ndi azikazi 80,
ndi anamwali osawerengeka;
9koma nkhunda yanga, wangwiro wanga ndi wosiyana ndi wina aliyense;
mwana wamkazi yekhayo wa amayi ake,
mwana wapamtima wa amene anamubereka.
Anamwali anamuona ndipo anamutcha wodala;
akazi a mfumu ndi azikazi anamutamanda.
Abwenzi

10Ndani uyu akuoneka ngati mʼbandakucha,
wokongola ngati mwezi, wowala ngati dzuwa,
wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili mʼmanja?
Mwamuna

11Ndinatsikira ku munda wa mitengo ya alimondi
kukayangʼana zomera zatsopano ku chigwa,
kukaona ngati mpesa waphukira
kapena ngati makangadza ali ndi maluwa.
12Ndisanazindikire kanthu,
ndinakhala ngati ndikulota kuti ndili mʼgaleta pambali pa mfumu yanga.
Abwenzi

13Bwerera, bwerera iwe namwali wa ku Sulami;
bwerera, bwerera kuti ife tidzakupenyetsetse iwe!
Mwamuna

Chifukwa chiyani mukufuna kudzapenyetsetsa ine mwana wamkazi wa ku Sulami,
pamene ndikuvina pakati pa magulu awiri?
Copyright information for NyaCCL